1 Samuel 15:23 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kugalukira kuli ngati tchimo loombeza, kukhala wokanika kuli ngati tchimo lopembedza mafano. Popeza kuti mwakana mau a Chauta, Iyenso wakukanani kuti musakhalenso mfumu.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti kupanduka kuli ngati choipa cha kuchita nyanga, ndi mtima waliuma uli ngati kupembedza milungu yachabe ndi maula. Popeza inu munakaniza mau a Yehova, Iyenso anakaniza inu, kuti simudzakhalanso mfumu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pakuti kuwukira kuli ngati tchimo lowombeza, ndipo kukhala nkhutukumve kuli ngati tchimo lopembedza mafano. Chifukwa mwakana mawu a Yehova. Iyenso wakukana kuti iweyo ukhale mfumu.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti kupanduka kuli ngati coipa ca kucita nyanga, ndi mtima waliuma uli ngati kupembedza milungu yacabe ndi maula. Popeza inu munakaniza mau a Yehova, Iyenso anakaniza inu, kuti simudzakhalanso mfumu.