1 Samuel 15:24 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamenepo Saulo adauza Samuele kuti, “Ndachimwa, ndalakwira lamulo la Chauta ndiponso malangizo anu, chifukwa chakuti ndinkaopa anthu ndipo ndinkamvera mau ao.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Saulo anati kwa Samuele, Ndinachimwa; pakuti ndinalumpha lamulo la Yehova, ndi mau anu omwe; chifukwa ndinaopa anthuwo, ndi kumvera mau ao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono Sauli anati kwa Samueli, “Ine ndachimwa. Ndaphwanya malamulo a Yehova ndiponso malangizo anu. Ndinkaopa anthu ndipo ndinawamvera.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Sauli anati kwa Samueli, Ndinacimwa; pakuti ndinalumpha lamulo la Yehova, ndi mau anu omwe; cifukwa ndinaopa anthuwo, ndi kumvera mau ao.