1 Samuel 15:26 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma Samuele adayankha kuti, “Sindibwerera nanu, popeza kuti mwakana mau a Chauta, Iyenso wakukanani kuti musakhalenso mfumu yolamulira Aisraele.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Samuele ananena ndi Saulo, Ine sindibwerera nanu; pakuti munakaniza mau a Yehova, ndipo Yehova anakaniza inu, kuti simudzakhalanso mfumu ya Israele.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma Samueli anawuza Sauli kuti, “Ine sindibwerera nawe. Inu mwakana mawu a Yehova. Choncho Iyenso wakukanani kuti musakhale mfumu yolamulira Aisraeli.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Samueli ananena ndi Sauli, Ine sindibwerera nanu; pakuti munakaniza mau a Yehova, ndipo Yehova anakaniza inu, kuti simudzakhalanso mfumu ya Israyeli.