1 Samuel 15:3 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pitani tsono, mukaŵathire nkhondo Aamalekewo, mukaononge kwathunthu zinthu zao zonse. Musakasiyeko munthu ndi mmodzi yemwe, mukaphe amuna, akazi, ana ndi makanda omwe. Mukaphenso ng'ombe, nkhosa, ngamira ndi abulu onse.’ ”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Muka tsopano, nukanthe Amaleke, nuononge konsekonse zonse ali nazo, usawalekerere, koma uwaphe mwamuna ndi mkazi, mwana ndi woyamwa, ng'ombe ndi nkhosa, ngamira ndi bulu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsopano pita kathire nkhondo Aamaleki ndi kuwononga kwathunthu zinthu zonse zimene ali nazo. Musakasiyeko munthu ndi mmodzi yemwe. Mukaphe amuna ndi akazi, ana ndi makanda, ngʼombe ndi nkhosa, ngamira ndi abulu.’ ”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Muka tsopano, nukanthe Amaleki, nuononge konse konse zonse ali nazo, usawalekerere, koma uwaphe mwamuna ndi mkazi, mwana ndi woyamwa, ng'ombe ndi nkhosa, ngamila ndi buru.