1 Samuel 15:32 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pambuyo pake Samuele adauza Saulo kuti, “Bwera nayeni kuno Agagi uja, mfumu ya Aamaleke.” Ndipo Agagiyo adafika kwa Samuele mokondwa, chifukwa adati, “Ndithudi, zoŵaŵa za imfa zapita!”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Samuele anati, Bwerani naye kwa ine kuno Agagi mfumu ya Aamaleke. Ndipo Agagi anabwera kwa iye mokondwera. Nati Agagi, Zoonadi kuwawa kwa imfa kunapitirira.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka Samueli anati, “Bwera nayeni kuno Agagi, mfumu ya Amaleki ija.” Choncho Agagi anapita kwa Samueli mokondwa chifukwa ankaganiza kuti, “Ndithu zowawa za imfa zapita.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Samueli anati, Bwerani naye kwa ine kuno Agagi mfumu ya Aamaleki. Ndipo Agagi anabwera kwa iye mokondwera. Nati Agagi, Zoonadi kuwawa kwa imfa kunapitirira.