1 Samuel 15:33 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma Samuele adati, “Monga momwe lupanga lako lasandutsira akazi kuti akhale opanda ana, momwemonso mai wako adzakhala wopanda mwana pakati pa akazi ena.” Ndipo Samuele adapha Agagiyo namduladula patsogolo pa guwa la Chauta ku Giligala.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Samuele anati, Monga lupanga lako linachititsa akazi ufedwa, momwemo mai wako adzakhala mfedwa mwa akazi. Ndipo Samuele anamdula Agagi nthulinthuli pamaso pa Yehova ku Giligala.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma Samueli anati, “Monga momwe lupanga lako linasandutsira amayi kukhala wopanda ana, momwemonso amayi ako adzakhala opanda mwana pakati pa amayi.” Ndipo Samueli anapha Agagi pamaso pa Yehova ku Giligala.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Samueli anati, Monga lupanga lako linacititsa akazi ufedwa, momwemo mai wako adzakhala mfedwa mwa akazi. Ndipo Samueli anamdula Agagi nthuli nthuli pamaso pa Yehova ku Giligala.