1 Samuel 15:6 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono adauza Akeni kuti, “Muchoke pakati pa Aamaleke, kuti ndingakuwonongereni kumodzi. Pakuti inu mudachitira chifundo Aisraele muja ankachokera ku Ejipitomu.” Motero Akeni adachoka pakati pa Aamaleke.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Saulo anauza Akeni kuti, Mukani, chokani mutsike kutuluka pakati pa Aamaleke, kuti ndingakuonongeni pamodzi ndi iwo; pakuti inu munachitira ana a Israele onse zabwino, pakufuma iwo ku Ejipito. Chomwecho Akeni anachoka pakati pa Aamaleke.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono Sauli anawuza Akeni kuti, “Samukani, muchoke pakati pa Aamaleki kuti ine ndisakuwonongeni pamodzi ndi iwo pakuti inu munaonetsa kukoma mtima kwa Aisraeli onse pamene ankatuluka mʼdziko la Igupto,” Choncho Akeni anachoka pakati pa Aamaleki.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Sauli anauza Akeni kuti, Mukani, cokani mutsike kuturuka pakati pa Aamaleki, kuti ndingakuonongeni pamodzi ndi iwo; pakuti inu munacitira ana a Israyeli onse zabwino, pakufuma iwo ku Aigupto. Comwece Akeni anacoka pakati pa Aamaleki.