1 Samuel 15:9 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma Saulo ndi anthu amene anali nawo, sadamuphe Agagi, sadaphenso nkhosa ndi ng'ombe zabwino koposa, anaang'ombe ndi anaankhosa onenepa, ndi zonse zimene zinkaoneka zabwino. Adangoononga zimene zinali zopanda ntchito ndi zachabechabe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma Saulo ndi anthu anamsunga wamoyo Agagi, ndi nkhosa zokometsetsa, ndi ng'ombe, ndi zonenepa zina, ndi anaankhosa, ndi zabwino zonse sadafuna kuzitha psiti; koma zonse zoipa ndi zonyansa anaziononga konsekonse.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma Sauli ndi ankhondo ake sanaphe Agagi, sanaphenso nkhosa ndi ngʼombe zabwino ngakhalenso ana angʼombe ndi ana ankhosa onenepa. Chilichonse chimene chinali chabwino sanachiphe. Koma zonse zimene zinali zoyipa ndi zachabechabe anaziwononga.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma Sauli ndi anthu anamsunga wamoyo Agagi, ndi nkhosa zokometsetsa, ndi ng'ombe, ndi zonenepa zina, ndi ana a nkhosa, ndi zabwino zonse, sadafuna kuzitha psiti; koma zonse zoipa ndi zonyansa anaziononga konse konse.