1 Samuel 16:1 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta adauza Samuele kuti, “Kodi udzakhala ukumlirabe Saulo mpaka liti, poti ndamkana kuti asakhalenso mfumu yolamulira Aisraele? Dzaza mafuta m'nsupa yakoyi. Upite kwa Yese wa ku Betelehemu, poti ndadzipezera mfumu pakati pa ana ake aamuna.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Yehova ananena ndi Samuele, Iwe ukuti ulire chifukwa cha Saulo nthawi yotani, popeza Ine ndinamkana kuti asakhale mfumu ya Israele? Dzaza nyanga yako ndi mafuta, numuke, ndidzakutumiza kwa Yese wa ku Betelehemu; pakuti ndinadzionera mfumu pakati pa ana ake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova anati kwa Samueli, “Kodi udzamulira Sauli mpaka liti, popeza Ine ndamukana kuti akhale mfumu ya Israeli? Dzaza mafuta mʼbotolo lako ndipo unyamuke kupita kwa Yese wa ku Betelehemu popeza ndadzisankhira mmodzi mwa ana ake kukhala mfumu.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Yehova ananena ndi Samueli, Iwe ukuti ulire cifukwa ca Sauli nthawi yotani, popeza Ine ndinamkana kuti asakhale mfumu ya Israyeli? Dzaza nyanga yako ndi mafuta, numuke, ndidzakutumiza kwa Jese wa ku Betelehemu; pakuti ndinadzionera mfumu pakati pa ana ace.