1 Samuel 16:10 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Choncho Yese adatumiza ana ake aamuna asanu ndi aŵiri kuti apite kwa Samuele. Koma Samueleyo adati, “Chauta sadaŵasankhe ameneŵa.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Yese anapititsapo ana ake amuna asanu ndi awiri. Koma Samuele anati kwa Yese, Yehova sanawasankhe awa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pambuyo pake, Yese anayitana ana ake amuna asanu ndi awiri kuti apite kwa Samueli. Koma Samueli anati, “Yehova sanasankhe amenewa.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Jese anapititsapo ana ace amuna asanu ndi awiri. Koma Samueli anati kwa Jese, Yehova sanawasankha awa.