1 Samuel 16:11 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono adafunsa Yese kuti, “Kodi ana ako aamuna ndi okhaŵa?” Yeseyo adati, “Alipo wina wamng'ono, mzime, amene watsala, koma iyeyo akuŵeta nkhosa.” Apo Samuele adauza Yese kuti, “Mtumireni munthu, akamtenge, pakuti sitipereka nsembe mpaka iyeyo atabwera pano”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Samuele anati kwa Yese, Ana anu ndi omwewa kodi? Nati iye, Watsala wina, mng'ono wa onse, ndipo taonani, iye alikuweta nkhosa. Ndipo Samuele anati kwa Yese, Tumiza munthu akamtenge; pakuti ife sitidzakhala pansi kufikira iye atadza kuno.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono Samueli anafunsa Yese kuti, “Kodi awa ndi ana ako onse aamuna?” Yese anayankha kuti, “Ayi, alipo wina wamngʼono amene watsala, koma akuweta nkhosa.” Samueli anati, “Apite munthu akamutenge popeza sitipereka nsembe mpaka iye atabwera.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Samueli anati kwa Jese, Ana anu ndi omwewa kodi? Nati iye, Watsala wina, mng'ono wa onse, ndipo taonani, iye alikuweta nkhosa. Ndipo Samueli anati kwa Jese, Tumiza munthu akamtenge; pakuti ife sitidzakhala pansi kufikira iye atadza kuno.