1 Samuel 16:12 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Choncho adatuma munthu kukamtenga, ndipo adabwera naye. Anali wofiirira ndi wa maonekedwe okongola ochititsa kaso. Pamenepo Chauta adati, “Ndi ameneyu, mdzoze.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anatumiza munthu, nabwera naye. Tsono iye anali wofiirira, ndi wa nkhope yokongola, ndi maonekedwe okoma. Ndipo Yehova anati, Nyamuka umdzoze, pakuti ndi ameneyu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho anatuma munthu kukamutenga ndipo anabwera naye. Iye anali wofiirira, wa maonekedwe abwino ochititsa kaso. Ndipo Yehova anati, “Mudzoze popeza ndi ameneyu.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anatumiza munthu, nabwera naye. Tsono iye anali wofiirira, ndi wa nkhope yokongola, ndi maonekedwe okoma. Ndipo Yehova anati, Nyamuka umdzoze, pakuti ndi ameneyu.