1 Samuel 16:13 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Samuele adatenga nsupa ya mafuta, namdzoza pamaso pa abale ake. Ndipo mzimu wa Chauta udamloŵa Davide mwamphamvu kuyambira tsiku limenelo mpaka m'tsogolo mwake. Pambuyo pake Samuele adanyamuka napita ku Rama.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo Samuele anatenga nyanga ya mafuta, namdzoza pakati pa abale ake; ndipo mzimu wa Yehova unalimbika pa Davide kuyambira tsiku lomweli. Ndipo Samuele ananyamuka, nanka ku Rama.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Samueli anatenga botolo la mafuta ndi kumudzoza pamaso pa abale ake, ndipo Mzimu wa Yehova unabwera mwamphamvu pa Davide kuyambira tsiku limenelo mpaka mʼtsogolo. Pambuyo pake Samueli anabwerera ku Rama.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo Samueli anatenga nyanga ya mafuta, namdzoza pakati pa abale ace; ndipo mzimu wa Yehova unalimbika pa Davide kuyambira tsiku lomweli. Ndipo Samueli ananyamuka, Danks ku Rama.