1 Samuel 16:18 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mmodzi mwa antchitowo adati, “Ndaona mwana wamwamuna wa Yese wa ku Betelehemu amene ali wokhoza zeze, munthu wolimba mtima, ngwazi pankhondo, wochenjera polankhula, munthu wokongola. Ndipo Chauta ali naye.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mnyamata wake wina anayankha, nati, Taonani, ine ndaona mwana wa Yese wa ku Betelehemu, ndiye wanthetemya wodziwa kuimbira, ndipo ali wa mtima wolimba ndi woyenera nkhondo, ndiponso ali wochenjera manenedwe ake; ndiye munthu wokongola, ndipo Yehova ali naye.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mmodzi mwa antchito ake anati, “Ine ndinaona mwana wa Yese wa ku Betelehemu. Ndiye munthu wodziwa bwino kuyimba, wolimba mtima, ngwazi pa nkhondo, wodziwa kuyankhula ndi wokongola. Ndipotu Yehova ali ndi iye.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mnyamata wace wina anayankha, nati, Taonani, ine ndaona mwana wa Jese wa ku Betelehemu, ndiye wanthetemya wodziwa kuyimbira, ndipo ali wa mtima wolimba ndi woyenera nkhondo, ndiponso ali wocenjera manenedwe ace; ndiye munthu wokongola, ndipo Yehova ali naye.