1 Samuel 16:20 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Yese adatenga bulu namsenzetsa buledi, thumba lachikopa la vinyo ndi mwanawambuzi. Zonsezo adapatsa Davide mwana wake, kuti akazipereke kwa Saulo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Yese anatenga bulu namsenza mkate, ndi thumba la vinyo, ndi mwanawambuzi, nazitumiza kwa Saulo ndi Davide mwana wake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho Yese anatenga bulu namunyamulitsa buledi, thumba la vinyo ndi mwana wambuzi mmodzi. Zonsezi anamupatsa mwana wake Davide kuti akapereke kwa Sauli.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Jese anatenga buru namsenza mkate, ndi thumba la vinyo, ndi: mwana wa mbuzi, nazitumiza kwa Sauli ndi Davide mwana wace.