1 Samuel 17:12 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Davide anali mwana wa Mwefurati wa ku Betelehemu dzina lake Yese, amene anali ndi ana aamuna asanu ndi atatu. Pa nthaŵi ya ufumu wa Saulo, Yese anali atakalamba kale kwambiri.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Tsono Davide anali mwana wa Mwefurati uja wa ku Betelehemu-Yuda, dzina lake ndiye Yese; ameneyu anali nao ana amuna asanu ndi atatu; ndipo m'masiku a Saulo munthuyo anali nkhalamba, mwa anthu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Davide anali mwana wa munthu wa fuko la Efurati dzina lake Yese amene amachokera ku Betelehemu mʼdziko la Yuda. Yese anali ndi ana aamuna asanu ndi awiri. Pa nthawi ya Sauli nʼkuti ali wokalamba.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Tsono Davide anali mwana wa M-efrati uja wa ku Betelehemu-Yuda, dzina lace ndiye Jese; ameneyu anali nao ana amuna asanu ndi atatu; ndipo m'masiku a Sauli munthuyo anali nkhalamba, mwa anthu.