1 Samuel 17:13 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ana ake aamuna anali aŵa: Eliyabu mwana wake wachisamba, wachiŵiri Abinadabu, ndipo wachitatu anali Sama.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ana atatu akulu a Yese anatsata Saulo kunkhondoko; ndi maina ao a ana ake atatuwo adapita ku nkhondowo ndiwo Eliyabu woyambayo, ndi mnzake womponda pamutu pake Abinadabu, ndi wachitatu Sama.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ana atatu oyamba kubadwa a Yese nʼkuti atapita nawo ku nkhondo pamodzi ndi Sauli. Woyamba dzina lake anali Eliabu, wachiwiri anali Abinadabu, ndipo wachitatu anali Sama.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ana atatu akuru a Jese anatsata Sauli kunkhondoko; ndi maina ao a ana ace atatuwo adapita ku nkhondowo ndiwo Eliabu woyambayo, ndi mnzace womponda pamutu pace Abinadabu, ndi wacitatu Sama.