1 Samuel 17:2 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Saulo adasonkhanitsa Aisraele, namanga zithando zao zankhondo m'chigwa cha Ela, nandanditsa gulu lankhondo kuti amenyane ndi Afilistiwo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Saulo ndi anthu a Israele anasonkhana, namanga zithando pa chigwa cha Ela, nandandalitsa nkhondo yao kuti akaponyane ndi Afilisti.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Sauli ndi Aisraeli anasonkhana namanga misasa mʼchigwa cha Ela ndipo anandandalitsa ankhondo kuti amenyane ndi Afilisti.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Sauli ndi anthu a Israyeli anasonkhana, namanga zithando pa cigwa ca Ela, nandandalitsa nkhondo yao kuti akaponyane ndi Afilisti.