1 Samuel 17:20 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Davide adanyamuka m'mamaŵa, nasiyira nkhosa munthu wina wozisunga. Adatenga zakudyazo napita, monga momwe bambo wake adaamlamulira. Adafika ku zithando pamene ankhondo ankandanda pa mzere wankhondo, nkufuula mfuu wankhondo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Davide anauka m'mamawa, nasiyira nkhosa wozisungira, nasenza zija, namuka, monga anamuuza Yese; ndipo iye anafika ku linga la magaleta, napeza khamu lilikutuluka kunka poponyanira nkhondo lilikufuula.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mʼmamawa mwake Davide anasiya nkhosa mʼmanja mwa munthu wina ndipo anatenga zakudyazo nanyamuka monga momwe Yese abambo ake anamulamulira. Anakafika ku misasa pamene asilikali ankapita kukandanda pa mzere ku nkhondo, nʼkufuwula mfuwu wankhondo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Davide anauka m'mamawa, nasiyira nkhosa wozisungira, nasenza zija, namuka, monga anamuuza Jese; ndipo iye anafika ku linga la magareta, napeza khamu lirikuturuka kunka poponyanira nkhondo lirikupfuula.