1 Samuel 17:23 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamene ankalankhula ndi abale akewo, adangoona Goliyati uja akutuluka ku magulu ankhondo a Afilisti, akulankhula zonyoza zomwe zija. Davide nkumva zimenezo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo m'mene iye anali chilankhulire nao, onani chinakwerako chiwindacho, Mfilisti wa ku Gati, dzina lake Goliyati, wotuluka pakati pa mipambo ya Afilisti, nalankhula monga mau omwe aja; ndipo Davide anawamva.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamene iye ankayankhula nawo anangoona Goliati wa ku Gati uja akuchoka pa mzere wa Afilisti akufuwula mawu onyoza monga mwa masiku onse, ndipo Davide ankawamva.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo m'mene iye anali cilankhulire nao, onani cinakwerako ciwindaco, Mfilisti wa ku Gati, dzina lace ndiye Goliate, woturuka pakati pa mipambo ya Afilisti, nalankhula monga mau omwe aja; ndipo Davide anawamva.