1 Samuel 17:25 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ankati, “Muwonenitu munthu uja! Amangobwera, amangodzatinyoza Aisraelefe. Tsono amene amuphe, mfumu idati idzampatsa chuma chambiri, adzampatsanso mwana wake wamkazi kuti amkwatire. Banja la bambo wake silidzalipiranso msonkho.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nati Aisraele, Kodi mwaona munthu uyu amene anakwera kuno? Zoonadi iye anakwera kuti adzanyoze Israele, ndipo munthu wakumupha iye, mfumu idzamlemeza ndi chuma chambiri, nidzampatsa mwana wake wamkazi, nidzayesa nyumba ya atate wake yaufulu m'Israele.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo Aisraeli ankanena kuti, “Kodi mwamuona munthu akubwerayo? Iye amangobwera kudzanyoza Israeli. Tsono mfumu inati kuti idzapereka chuma chambiri kwa munthu amene adzamuphe. Idzaperekanso mwana wake wamkazi kuti amukwatire ndiponso banja la abambo ake silidzaperekanso msonkho mu Israeli.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nati Aisrayeli, Kodi mwaona munthu uyu amene anakwera kuno? zoonadi iye anakwera kuti adzanyoze Israyeli, ndipo munthu wakumupha iye, mfumu idzamlemeza ndi cuma cambiri, nidzampatsa mwana wace wamkazi, nidzayesa nyumba ya atate wace yaufulu m'Israyeli.