1 Samuel 17:26 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Davide adafunsa anthu amene anali pafupi naye kuti, “Adzamtani munthu amene adzaphe Mfilistiyu ndi kuŵachotsa manyazi Aisraele? Mfilisti wosaumbalidwayu ndaninso kuti angamanyoze ankhondo a Mulungu wamoyo?”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Davide analankhula ndi anthu akuima pafupi ndi iye, nati, Adzamchitira chiyani munthu wakupha Mfilisti uyu, ndi kuchotsa tonzo lake pakati pa Israele? Pakuti Mfilisti uyu wosadulidwa ndiye yani, kuti azinyoza makamu a Mulungu wamoyo?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Davide anafunsa anthu amene anayima pafupi naye kuti, “Kodi adzamuchita chiyani munthu amene adzapha Mfilisiti uyu ndi kuchotsa chitonzo pakati pa Israeli? Mfilisiti wosachita mdulidweyu ndi ndani kuti azinyoza gulu lankhondo la Mulungu wamoyo?”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Davide analankhula ndi anthu akuima pafupi ndi iye, nati, Adzamcitira ciani munthu wakupha Mfilisti uyu, ndi kucotsa tonzo lace pakati pa Israyeli? pakuti Mfilisti uyu wosadulidwa ndiye yani, kuti azinyoza makamu a Mulungu wamoyo?