1 Samuel 17:3 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Afilisti ndi Aisraele adaika ankhondo ao moyang'anana, ena mbali ina paphiri, ena mbali ina paphirinso, pakatipa chigwa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Afilisti anaima paphiri tsidya lija, ndi Aisraele anaima paphiri tsidya lina; ndi pakati pao panali chigwa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Afilisti anali phiri lina ndipo Aisraeli analinso phiri lina, ndipo pakati pawo panali chigwa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Afilisti anaima paphiri tsidya lija, ndi Aisrayeli anaima paphiri tsidya lina; ndi pakati pao panali cigwa.