1 Samuel 17:35 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
ndinkalondola mpaka kuchipha chilombocho ndi kupulumutsa mwanawankhosayo kukamwa kwake. Ndipo chikati chindiwukire, ndinkachigwira tchoŵa lake ndi kuchikantha mpaka kuchipha.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndinachithamangira, ndi kuchikantha, ndi kuitulutsa m'kamwa mwake; ndipo pamene chinandiukira, ndinagwira tchowa lake ndi kuchikantha ndi kuchipha.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
ine ndinkatsatira ndi kupha chirombocho. Choncho ndinkapulumutsa mwana wankhosa uja mʼkamwa mwake. Ndipo chinkati chikandiwukira, ine ndinkagwira tchowa lake, nʼkuchikantha mpaka kuchipha.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndinacithamangira, ndi kucikantha, ndi kuiturutsa m'kamwa mwace; ndipo pamene cinaneliukira, ndinagwira cowa lace ndi kucikantha ndi kucipha.