1 Samuel 17:36 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ineineyo ndidaphapo mikango ndi zimbalangondo zomwe. Tsono Mfilisti wosaumbalidwayu, ndidzamupha monga momwe ndidaphera zilombo zija, popeza kuti akunyoza magulu ankhondo a Mulungu wamoyo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ine kapolo wanu ndinapha mkango ndi chimbalangondo zonse ziwiri; ndipo Mfilisti uyu wosadulidwa adzakhala ngati mmodzi wa izo, popeza wanyoza makamu a Mulungu wamoyo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ine kapolo wanu ndinapha mkango ngakhalenso chimbalangondo. Tsono Mfilisiti wosachita mdulidweyu adzaphedwa monga zinazo chifukwa wanyoza ankhondo a Mulungu wamoyo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ine kapolo wanu ndinapha mkango ndi cimbalangondo zonse ziwiri; ndipo Mfilisti uyu wosadulidwa adzakhala ngati mmodzi wa izo, popeza wanyoza makamu a Mulungu wamoyo.