1 Samuel 17:37 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta amene adandipulumutsa ku mkango ndi ku chimbalangondo, adzandipulumutsa kwa Mfilistiyu.” Apo Saulo adauza Davide kuti, “Pita, Chauta akhale nawe.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nati Davide, Yehova wakundipulumutsa pa mphamvu ya mkango, ndi mphamvu ya chimbalangondo, Iyeyu adzandipulumutsa m'dzanja la Mfilisti uyu. Ndipo Saulo anati kwa Davide, Muka, Yehova akhale nawe.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova amene anandilanditsa mʼkamwa mwa mkango ndi chimbalangondo adzandilanditsa mʼmanja mwa Mfilisiti uyu.” Sauli anati kwa Davide, “Pita, ndipo Yehova akhale nawe.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nati Davide, Yehova wakundipulumutsa pa mphamvu ya mkango, ndi mphamvu ya cimbalangondo, Iyeyu adzandipulumutsa m'dzanja la Mfilisti uyu, Ndipo Sauli anati kwa Davide, Muka, Yehova akhale nawe.