1 Samuel 17:39 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kenaka Davide adamanga lupanga m'chiwuno mwake. Atayesera kuyenda, adaona kuti akulephera poti sadazoloŵere. Ndiye adauza Saulo kuti, “Sindingathe kuyenda nazo, poti sindidazoloŵere.” Choncho adavula zovalazo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Davide anamanga lupanga lake pamwamba pa zovala zake, nayesa kuyenda nazo; popeza sanaziyesera kale. Ndipo Davide anati kwa Saulo, Sindikhoza kuyenda ndi izi; pakuti sindinazizolowera. Nazivula Davide.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Davide anamangirira lupanga pa mwinjirowo. Atayesa kuyenda nazo, analephera chifukwa anali asanazizolowere. Iye anati kwa Sauli, “Sindingathe kuyenda nazo chifukwa sindinazizolowere.” Ndipo anazivula.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Davide anamanga lupanga lace pamwamba pa zobvala zace, nayesa kuyenda nazo; popeza sanaziyesera kale. Ndipo Davide anati kwa Sauli, Sindikhoza kuyenda ndi izi; pakuti sindinazizolowera. Nazibvula Davide.