1 Samuel 17:4 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono ku zithando za Afilisti kudatuluka munthu wina wamphamvu wa ku Gati, dzina lake Goliyati. Msinkhu wake unali pafupi mamita atatu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ku zithando za Afilisti kunatuluka chiwinda, dzina lake Goliyati wa ku Gati, kutalika kwake ndiko mikono isanu ndi umodzi ndi dzanja limodzi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono munthu wina wamphamvu, dzina lake Goliati wochokera ku Gati anatuluka ku misasa ya Afilisti. Msinkhu wake unali pafupipafupi mamita atatu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ku zithando za Afilisti kunaturuka ciwinda, dzina lace Goliate wa ku Gati, kutalika kwace ndiko mikono isanu ndi umodzi ndi cikhato.