1 Samuel 17:40 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono adatenga ndodo yake m'manja. Adatola miyala isanu yosalala yakumtsinje, naiika m'thumba lake lakubusa. Ali ndi khwenengwe m'manja, adapita kukakumana ndi Mfilisti uja.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Natenga ndodo yake m'dzanja lake nadzisankhira miyala isanu yosalala ya mumtsinje, naiika m'thumba la kubusa, limene anali nalo ndilo chibete; ndi choponyera miyala chinali m'dzanja lake, momwemo anayandikira kwa Mfilistiyo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pambuyo pake anatenga ndodo yake mʼmanja. Kenaka anasankha miyala yosalala bwino mu mtsinje ndi kuyiika mʼthumba lake la ku ubusa. Legeni ili mʼmanja mwake, Davide ananyamuka kukakumana ndi Mfilisiti uja.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Natenga ndodo yace m'dzanja lace nadzisankhira miyala isanu yosalala ya mumtsinje, naiika m'thumba la kubusa, limene anali nalo ndilo cibete; ndi coponyera miyala cinali m'dzanja lace, momwemo anayandikira kwa Mfilistiyo.