1 Samuel 17:42 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndipo atayang'ana Davideyo, adayamba kumnyoza, poona kuti anali mnyamata chabe, wofiirira ndiponso wa maonekedwe okongola.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Mfilisti pakumwazamwaza maso, ndi kuona Davide, anampeputsa; popeza anali mnyamata chabe, wofiirira, ndi wa nkhope yokongola.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mfilisitiyo atangomuona Davide, anamunyoza popeza kuti Davide anali mnyamata chabe wofiirira ndi wa maonekedwe abwino.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Mfilisti pakumwazamwaza maso, ndi kuona Davide, anampeputsa; popeza anali mnyamata cabe, wofiirira, ndi wa nkhope yokongola.