1 Samuel 17:46 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Lero lomwe lino Chauta akupereka m'manja mwanga. Ndikulasa ndi kukugwetsa pansi, ndipo ndikudula mutu. Mitembo ya magulu ankhondo a Afilisti ndiipereka lero lino kwa mbalame zamumlengalenga, ndi kwa zilombo zakuthengo, kuti dziko lonse lapansi lidziŵe kuti kuli Mulungu ku dziko la Israele.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Lero lino Yehova adzakupereka iwe m'dzanja langa, ndipo ndidzakukantha, ndi kukuchotsera mutu wako. Ndipo lero ndidzapatsa mitembo ya makamu a Afilisti kwa mbalame za mlengalenga, ndi kwa zilombo za dziko lapansi; kuti dziko lonse likazindikire kuti kwa Israele kuli Mulungu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anatinso lero lino Yehova adzakupereka mʼmanja mwanga. Ndidzakukantha ndi kudula mutu wako. Ndidzapereka mitembo ya asilikali a Afilisti kwa mbalame za mlengalenga, ndi kwa zirombo zakuthengo ndipo dziko lonse lapansi lidzadziwa kuti mu Israeli muli Mulungu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Lero lino Yehova adzakupereka iwe m'dzanja langa, ndipo ndidzakukantha, ndi kukucotsera mutu wako. Ndipo lero ndidzapatsa mitembo ya makamu a Afilisti kwa mbalame za mlengalenga, ndi kwa zirombo za dziko lapansi; kuti dziko lonse likazindikire kuti kwa Israyeli kuli Mulungu.