1 Samuel 17:47 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthu onse amene asonkhanaŵa adzadziŵa kuti Chauta sapulumutsa anthu ndi lupanga kapena mkondo wokha. Wopambanitsa pa nkhondo ndi Chauta, ndipo akuperekani m'manja mwathu.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndi msonkhano wonse uno udzazindikira kuti Yehova sapulumutsa ndi lupanga, kapena ndi mkondo; pakuti Yehova ndiye mwini nkhondo, ndipo Iye adzakuperekani inu m'manja athu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Onse amene asonkhana pano adzadziwa kuti Mulungu sapulumutsa anthu ndi lupanga kapena mkondo, pakuti nkhondo ndi ya Yehova. Iye adzakuperekani mʼmanja mwathu.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndi msonkhano wonse uno udzazindikira kuti Yehova sapulumutsa ndi lupanga, kapena ndi mkondo; pakuti Yehova ndiye mwini nkhondo, ndipo iye adzakuperekani inu m'manja athu.