1 Samuel 17:50 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Choncho Davide adampambana Goliyati uja pomlasa ndi mwala wam'khwenengwe, namupha Mfilistiyo. M'manja mwa Davide munalibe konse lupanga.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chomwecho Davide anapambana Mfilistiyo ndi mwala wa choponyera chake, nakantha Mfilistiyo, namupha. Koma m'dzanja la Davide munalibe lupanga.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kotero Davide anamupambana Mfilisitiyo pomugenda ndi mwala wa legeni ndi kumupha. Mʼmanja mwa Davide munalibe lupanga.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Comweco Davide anapambana Mfilistiyo ndi mwala wa coponyera cace, nakantha Mfilistiyo, namupha. Koma m'dzanja la Davide munalibe lupanga.