1 Samuel 17:51 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pompo adathamanga, nakaimirira pamwamba pa Mfilisti uja. Adasolola lupanga lake lomwe m'chimake, namtsiriza pomdula mutu. Tsono Afilisti ataona kuti ngwazi yao yamphamvu pa nkhondo yafa, adathaŵa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Potero Davide anathamanga naima pa Mfilistiyo, nagwira lupanga lake, nalisolola m'chimake, namtsiriza nadula nalo mutu wake. Ndipo pakuona Afilisti kuti chiwinda chao chidafa, anathawa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Davide anathamanga nakayimirira pamwamba pa Mfilisiti uja. Anasolola lupanga lake lomwe moyikamo mwake, namupha pomudula mutu wake. Afilisti ataona kuti ngwazi yawo yafa, anathawa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Potero Davide anathamanga naima pa Mfilistiyo, nagwira lupanga lace, nalisolola m'cimace, namtsiriza nadula nalo mutu wace. Ndipo pakuona Afilisti kuti ciwinda cao cidafa, anathawa.