1 Samuel 17:52 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Aisraele ndi anthu a ku dziko la Yuda adanyamuka akufuula, napirikitsa Afilisti aja mpaka ku Gati ndi ku zipata za Ekeroni. Tsono Afilisti ovulala ankagwa pa njira yonse kuyambira ku Saraimu mpaka ku Gati ndi Ekeroni.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anthu a Israele ndi Ayuda ananyamuka, nafuula, nathamangira Afilistiwo, mpaka ufika kuchigwako, ndi ku zipata za Ekeroni. Ndipo Afilistiwo olasidwa anagwa pa njira ya ku Saaraimu, kufikira ku Gati ndi ku Ekeroni.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo Aisraeli ndi anthu a ku Yuda ananyamuka, ndipo akufuwula anathamangitsa Afilisti aja mpaka ku Gati ndi ku zipata za Ekroni. Anthu akufa awo amagwa njira yonse ya ku Saaraimu mpaka ku Gati ndi ku Ekroni.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anthu a Israyeli ndi Ayuda ananyamuka, napfuula, nathamangira Afilistiwo, mpaka ufika kucigwako, ndi ku zipata za Ekroni. Ndipo Afilistiwo olasidwa anagwa pa njira ya ku Saraimu, kufikira ku Gad ndi ku Ekroni.