1 Samuel 17:54 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kenaka Davide adatenga mutu wa Mfilisti uja napita nawo ku Yerusalemu. Koma zida zokha za Mfilistiyo adaziika m'hema mwake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Davide anatenga mutu wa Mfilistiyo, napita nao ku Yerusalemu; koma zida zake anazisunga m'hema wake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pambuyo pake Davide anatenga mutu wa Mfilisitiyo napita nawo ku Yerusalemu, koma anayika zida za Mfilisitiyo mu tenti yake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Davide anatenga mutu wa Mfilistiyo, napita nao ku Yerusalemu; koma zida zace anazisunga m'hema wace.