1 Samuel 17:55 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamene Saulo adaaona Davide akupita kukamenyana ndi Mfilisti uja, adafunsa Abinere mkulu wa ankhondo kuti, “Kodi iwe Abinere, mnyamatayu ndi mwana wa yani?” Abinere adayankha kuti, “Pepani inu amfumu muli apa, ine sindingadziŵe.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo pamene Saulo anaona Davide alikutulukira kwa Mfilistiyo, iye anati kwa Abinere, kazembe wa khamu la nkhondo, Abinere, mnyamata uyu ndi mwana wa yani? Nati Abinere, Pali moyo wanu, mfumu, ngati ndidziwa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Sauli ataona Davide akupita kukakumana ndi Mfilisitiyo anafunsa Abineri, mkulu wa ankhondo kuti, “Abineri, kodi mnyamatayu ndi mwana wa yani?” Abineri anayankha kuti, “Ndithu mfumu muli apa ine sindikumudziwa.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo pamene Sauli anaona Davide alikuturukira kwa Mfilistiyo, iye anati kwa Abineri, kazembe wa khamu la nkhondo, Abineri, mnyamata uyu ndi mwana wa yani? Nati Abineri, Pali moyo wanu, mfumu, ngati ndidziwa.