1 Samuel 17:57 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono pamene Davide ankabwererako kumene adaakapha Mfilisti kuja, Abinere adamtenga napita naye kwa Saulo, mutu wa Mfilisti uja uli m'manja mwake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo pamene Davide anabwera, atapha Mfilistiyo, Abinere anamtenga, nafika naye pamaso pa Saulo, mutu wa Mfilistiyo uli m'dzanja lake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Davide atangobwerako kokapha Mfilisiti kuja, Abineri anamutenga nabwera naye kwa Sauli, mutu wa Mfilisiti uja uli mʼmanja mwake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo pamene Davide anabwera, atapha Mfilistiyo, Abineri anamtenga, nafika naye pamaso pa Sauli, mutu wa Mfilistiyo uli m'dzanja lace.