1 Samuel 17:58 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Saulo adafunsa Davide kuti, “Kodi mnyamata iwe, paja ndiwe mwana wa yani?” Davide adayankha kuti, “Ndine mwana wa mtumiki wanu Yese, wa ku Betelehemu.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Saulo anati kwa iye, Mnyamata iwe, ndiwe mwana wa yani? Davide nayankha, Ndili mwana wa kapolo wanu Yese wa ku Betelehemu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Sauli anamufunsa, “Mnyamata iwe, kodi paja ndiwe mwana wayani?” Davide anati, “Ndine mwana wa mtumiki wanu Yese wa ku Betelehemu.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Sauli anati kwa iye, Mnyamata iwe, ndiwe mwana wa yani? Davide nayankha, Ndiri mwana wa kapolo wanu Jese wa ku Betelehemu.