1 Samuel 17:8 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Goliyatiyo adaimirira ndi kufuula kwa ankhondo a Aisraele kuti, “Chifukwa chiyani mukuchita kukonzekera nkhondo chotere? Ineyo ndine Mfilisti, inuyo ndinu akapolo a Saulo. Bwanji osati mungosankhula munthu pakati panupo, adze kwa ine.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Naima iye naitana makamu a nkhondo a Israele, nanena nao, Munatulukiranji kundandalitsa nkhondo yanu? Sindine Mfilisti kodi, ndi inu anyamata a Saulo? Mudzisankhire munthu, atsikire kwa ine.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Goliatiyo anayimirira ndi kufuwula kwa ankhondo a Israeli, nati, “Nʼchifukwa chiyani mwakonzekera nkhondo chotere? Kodi sindine Mfilisiti ndipo inu sindinu akapolo a Sauli? Sankhani munthu kuti abwere kwa ine.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Naima iye naitana makamu a nkhondo a Israyeli, nanena nao, Munaturukiranji kundandalitsa nkhondo yanu? Sindine Mfilisti kodi, ndi inu anyamata a Sauli? mudzisankhire munthu, atsikire kwa ine.