1 Samuel 18:1 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Davide atatha kulankhula ndi Saulo, mtima wa Yonatani udagwirizana ndi mtima wa Davide, ndipo Yonatani adakonda Davideyo monga momwe ankadzikondera iye mwini.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo kunali, pakutsiriza iye kulankhula ndi Saulo, mtima wa Yonatani unalumikizika ndi mtima wa Davide, ndipo Yonatani anamkonda iye monga moyo wa iye yekha.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Davide atatha kuyankhula ndi Sauli, mtima wa Yonatani unagwirizana ndi mtima wa Davide, ndipo iye ankamukonda Davide monga momwe ankadzikondera yekha.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo kunali, pakutsiriza iye kulankhula ndi Sauli, mtima wa Jonatani unalumikizika ndi mtima wa Davide, ndipo Jonatani anamkonda iye monga moyo wa iye yekha.