1 Samuel 18:10 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
M'maŵa mwake mzimu woipa uja udamtsikira Saulo, ndipo adayamba kubwebweta moyaluka m'nyumba mwake. Davide ankamuimbira zeze, monga momwe ankachitira tsiku ndi tsiku. Saulo anali ndi mkondo m'manja mwake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo kunali m'mawa mwake, mzimu woipa wochokera kwa Mulungu unamgwira Saulo mwamphamvu, iye nalankhula moyaluka m'nyumba yake; koma Davide anaimba ndi dzanja lake, monga amachita tsiku ndi tsiku; koma m'dzanja la Saulo munali mkondo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mmawa mwake mzimu woyipa uja unabwera mwamphamvu pa Sauli. Sauli anayamba kubwebweta mʼnyumba mwake. Davide ankamuyimbira zeze monga nthawi zonse. Sauli anali ndi mkondo mʼdzanja lake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo kunali m'mawa mwace, mzimu woipa wocokera kwa Mulungu unamgwira Sauli mwamphamvu, iye nalankhula moyaruka m'nyumba yace; koma Davide anayimba ndi dzanja lace, monga amacita tsiku ndi tsiku; koma m'dzanja la Sauli munali mkondo.