1 Samuel 18:13 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Motero Saulo adamtuma Davide kwina kwake, ndipo adamuika kuti akhale mtsogoleri wa ankhondo 1,000. Davide ankapita namabwera akuŵatsogolera.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa chake Saulo anamchotsa kuti asakhale naye, namuika akhale mtsogoleri wake wa anthu chikwi chimodzi; ndipo iye anatsogolera anthu kutuluka ndi kubwera nao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kotero Sauli anamuchotsa Davide pamaso pake ndi kumuyika kukhala mtsogoleri wa ankhondo 1,000. Choncho Davide ankapita ndi kubwera akutsogolera ankhondowa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa cace Sauli anamcotsa kuti asakhale naye, namuika akhale mtsogoleri wace wa anthu cikwi cimodzi; ndipo iye anatsogolera anthu kuturuka ndi kubwera nao.