1 Samuel 18:17 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsiku lina Saulo adauza Davide kuti, “Nayu Merabi mwana wanga wamkulu. Ndidzakupatsa kuti akhale mkazi wako. Koma unditumikire molimba mtima pomenya nkhondo za Chauta.” Potero Saulo ankaganiza kuti, “Ndisamuphe ndine ndi dzanja langa, koma amuphe ndi Afilisti.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Saulo anati kwa Davide, Ona, mwana wanga wamkazi wamkulu, dzina lake Merabi, iyeyo ndidzakupatsa akhale mkazi wako; koma undikhalire ngwazi, nuponye nkhondo za Yehova. Pakuti Saulo anati, Dzanja langa lisamkhudze, koma dzanja la Afilisti ndilo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsiku lina Sauli anawuza Davide kuti, “Nayu Merabi mwana wanga wamkazi wamkulu. Ine ndakupatsa kuti umukwatire. Koma unditumikire molimba mtima pomenya nkhondo za Yehova.” Poteropo Sauli ankanena kuti, “Ndisamuphe ndi manja angawa koma aphedwe ndi Afilisti!”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Sauli anati kwa Davide, Ona, mwana wanga wamkazi wamkuru, dzina lace Merabi, iyeyo ndidzakupatsa akhale mkazi wako; koma undikhalire ngwazi, nuponye nkhondo za Yehova. Pakuti Sauli anati, Dzanja langa lisamkhudze, koma dzanja la Afilisti ndilo.