1 Samuel 18:19 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma pa nthaŵi yoti Merabi, mwana wa Saulo, akwatiwe ndi Davide, bambo wake adampereka kwa Adriyele Mmehola, kuti akhale mkazi wake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma kunali nthawi imene akadapatsa Merabi mwana wamkazi wa Saulo kwa Davide, iye anapatsidwa kwa Adriyele Mmehola kukhala mkazi wake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma pa nthawi yoti Merabi mwana wa Sauli akwatiwe ndi Davide, Sauli anamupereka kwa Adrieli wa ku Mehola kuti amukwatire.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma kunali nthawi imene akadapatsa Merabi mwana wamkazi wa Sauli kwa Davide, iye anapatsidwa kwa Adrieli Mholati kukhala mkazi wace.