1 Samuel 18:22 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Motero adalamula nduna zake kuti, “Mulankhule naye Davide pambali nkumuuza kuti, ‘Mfumu imakukonda, ndipo ngakhale nduna zake zimakukonda. Tsono ukhale mkamwini wa mfumu.’ ”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Saulo analamulira anyamata ake, nati, Mulankhule naye Davide m'tseri, ndi kuti, Taonani mfumu akondwera nanu, ndi anyamata ake onse akukondani; chifukwa chake tsono, khalani mkamwini wa mfumu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Sauli analamulanso nduna zake kuti, “Muyankhuleni Davide mwamseri ndi kumuwuza kuti, ‘Taona, mfumu imakondwera nawe, ndipo nduna zake zonse zimakukonda. Tsono ukhale mkamwini wa mfumu.’ ”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Sauli analamulira anyamata ace, nati, Mulankhule naye Davide m'tseri, ndi kuti, Taonani mfumu akondwera nanu, ndi anyamata ace onse akukondani; cifukwa cace tsono, khalani mkamwini wa mfumu.