1 Samuel 18:30 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono pamene Afilisti ankatuluka kukamenya nkhondo, nthaŵi zonse Davide ankapambana kwambiri kuposa atsogoleri ena onse a ankhondo a Saulo. Choncho dzina lake la Davide lidatchuka kwambiri.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pomwepo mafumu a Afilisti anatuluka; ndipo nthawi zonse anatuluka iwo, Davide anali wochenjera koposa anyamata onse a Saulo, chomwecho dzina lake linatamidwa kwambiri.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nthawi zonse pamene atsogoleri a Afilisti ankatuluka kukamenya nkhondo, Davide ankapambana kuposa nduna zonse za Sauli. Choncho dzina lake linatchuka kwambiri.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pomwepo mafumu a Afilisti anaturuka; ndipo nthawi zonse anaturuka iwo, Davide anali wocenjera koposa anyamata onse a Sauli, comweco dzina lace linatamidwa kwambiri.