1 Samuel 18:5 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono kulikonse kumene Davide ankatumidwa ndi Saulo kuti akamenye nkhondo, ankapambana adani. Motero Saulo adamuika Davide kuti akhale mtsogoleri wa ankhondo. Chimenechi chidakondwetsa anthu onse, ngakhalenso atsogoleri a ankhondo a Saulo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Davide anatuluka kunka kulikonse Saulo anamtumako, nakhala wochenjera; ndipo Saulo anamuika akhale woyang'anira anthu a nkhondo; ndipo ichi chinakomera anthu onse, ndi anyamata a Saulo omwe.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Davide ankapita kulikonse kumene Sauli ankamutuma kuti apite kukamenya nkhondo, ndipo ankapambana. Choncho Sauli anamupatsa udindo woyangʼanira gulu lankhondo. Ichi chinakondweretsa anthu onse ngakhalenso atsogoleri a nkhondo a Sauli.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Davide anaturuka kunka kuli konse Sauli anamtumako, nakhala wocenjera; ndipo Sauli anamuika akhale woyang'anira anthu a nkhondo; ndipo ici cinakomera anthu onse, ndi anyamata a Sauli omwe.