1 Samuel 18:6 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamene anthu ankabwerera kwao, Davide atapha Mfilisti uja, akazi adatuluka m'mizinda yonse ya Aisraele akuimba ndi kuvina, kuti achingamire mfumu Saulo. Ankaimba ndi kumavina mokondwa, kwinaku ng'oma ndi zitoliro zikugundika.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo kunali pakudza iwo, pamene Davide anabwera atapha Afilistiwo, anthu akazi anatuluka m'midzi yonse ya Israele, ndi kuimba ndi kuvina, kuti akakomane ndi mfumu Saulo, ndi malingaka, ndi chimwemwe, ndi zoimbira.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anthu akubwerera kwawo Davide atapha Mfilisiti uja, amayi anatuluka mʼmizinda yonse ya Israeli, akuyimba ndi kuvina kukachingamira mfumu Sauli. Ankayimba ndi kuvina mokondwa, kwinaku ngʼoma ndi zitoliro zikulira.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo kunali pakudza iwo, pamene Davide anabwera atapha Afilistiwo, anthu akazi anaturuka m'midzi yonse ya Israyeli, ndi kuyimba ndi kubvina, kuti akakomane ndi mfumu Sauli, ndi malingaka, ndi cimwemwe, ndi zoyimbira.