1 Samuel 19:1 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Saulo adalamula mwana wake Yonatani ndi akuluakulu onse kuti aphe Davide. Koma Yonatani ankakonda Davide kwambiri.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Saulo analankhula kwa Yonatani mwana wake, ndi anyamata ake onse kuti amuphe Davide.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Sauli anawuza mwana wake Yonatani ndi nduna zake zonse kuti aphe Davide. Koma Yonatani amamukonda kwambiri Davide.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Sauli analankhula kwa Jonatani mwana wace, ndi anyamata ace onse kuti amuphe Davide.